Muzigwiritsa Ntchito Webusaiti Yathu ya jw.org/ny Polalikira
Webusaiti yathu ndi yothandiza kwambiri polalikira uthenga wabwino “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Komatu anthu ambiri satha kupeza okha webusaitiyi pa Intaneti. Koma wofalitsa akawathandiza kudziwa mmene angaipezere, amayamba kuigwiritsa ntchito.
Woyang’anira dera anapanga dawunilodi vidiyo yakuti, N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? ndipo ali nayo pafoni yake. Woyang’anira derayu amaonetsa anthu vidiyoyi nthawi iliyonse yomwe wapeza mpata. Mwachitsanzo, polalikira kunyumba ndi nyumba wakumana ndi munthu wina ndipo akumuuza kuti: “Ndikucheza mwachidule ndi anthu kuwathandiza kuti athe kupeza mayankho a mafunso atatu ofunika kwambiri awa: N’chifukwa chiyani padzikoli pali mavuto ambiri chonchi? Kodi Mulungu adzawathetsa bwanji? Nanga n’chiyani chingatithandize kupirira padakali pano? Ndili ndi Vidiyo yachidule yomwe ingakuthandizeni kudziwa komwe mungapeze mayankho a mafunso amenewa.” Kenako akutsegula vidiyoyo n’kuyamba kumuonetsa ndipo akuona ngati munthuyo akusonyeza chidwi kapena ayi. Vidiyoyi ndi yochititsa chidwi kwambiri moti anthu ambiri akayamba kuionera, safuna kuisiya. Kenako woyang’anira derayo akuuza munthuyo kuti: “Monga mwamvera m’vidiyoyi, kudzera pa webusaiti yathu, mungathe kupempha kuti munthu aziphunzira nanu Baibulo. Choncho ngati mungakonde, ndingakusonyezeni mwachidule mmene timachitira phunziroli.” Munthuyo akuvomera, ndipo woyang’anira derayo akumusonyeza pogwiritsa ntchito kabuku kakuti, Uthenga Wabwino. Koma ngati munthuyo wanena kuti alibe nthawi yokwanira, apangane naye kuti adzabweranso kuti adzamusonyeze. Kenako woyang’anira derayo akuima penapake kuti amwe zakumwa zoziziritsa kukhosi komanso kuti apume pang’ono. Akupeza munthu wina pamalowo ndipo atacheza naye kwakanthawi, akumuuzanso zokhudza vidiyo ija ndipo akuchita zofanana ndi zimene anachita poyamba paja. Kodi inuyo mumagwiritsa ntchito webusaiti yathu ya jw.org/ny kuuza anthu uthenga wa m’Baibulo?