Akulalikira kwa mayi ndi mwana wake ku West Bengal m’dziko la India
Zitsanzo za Ulaliki
NSANJA YA OLONDA
Funso: Tonsefe timafunika kuthandizidwa tikakumana ndi mavuto. Koma kodi ndi ndani angatithandize tikakhala pamavuto?
Lemba: 2 Akor. 1:3, 4
Perekani Magaziniyo: Maganiziyi ikufotokoza zimene Mulungu amachita kuti atithandize tikakumana ndi mavuto.
NSANJA YA OLONDA (tsamba lomaliza)
Funso: Anthu ena amaganiza kuti Ufumu wa Mulungu uli mumtima mwa munthu, pomwe ena amaganiza kuti Ufumu wa Mulungu udzakhalapo anthu akadzakwanitsa kukhazikitsa mtendere ndiponso mgwirizano padzikoli. Inuyo mukuganiza bwanji?
Lemba: Dan. 2:44
Perekani Magaziniyo: Lembali likusonyeza kuti Ufumu wa Mulungu ndi boma lenileni. Nkhaniyi ikufotokozanso zinthu zina zimene Baibulo limanena zokhudza Ufumu wa Mulungu
KUPHUNZITSA CHOONADI
Funso: Kodi tingadziwe bwanji kuti Mulungu amatiganizira?
Lemba: 1 Pet. 5:7
Zoona Zake: Yehova amatiganizira, n’chifukwa chake amatiuza kuti tizipemphera kwa iye.
LEMBANI ULALIKI WANUWANU
Potengera zitsanzozi, konzani njira imene mungagwiritse ntchito.