Akulalikira mumsika ku Sierra Leone
Zitsanzo za Ulaliki
GALAMUKANI!
Funso: Kodi n’chifukwa chiyani zinthu m’dzikoli zikuipiraipira?
Lemba: Yer. 10:23
Perekani Magaziniyo: Magazini iyi ikufotokoza chifukwa chake anthu ambiri amakhulupirira kuti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolomu.
GALAMUKANI!
Funso: Kodi Mulungu ali ndi dzina?
Lemba: Sal. 83:18
Perekani Magaziniyo: Nkhani iyi ikufotokoza zimene dzina la Mulungu limatanthauza komanso chifukwa chake tiyenera kumaligwiritsa ntchito. [Tsegulani pamene pali nkhani yakuti, “Zimene Baibulo Limanena—Dzina la Mulungu.”]
KUPHUNZITSA CHOONADI
LEMBANI ULALIKI WANUWANU
Potengera zitsanzozi, konzani njira imene mungagwiritse ntchito.