CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YESAYA 24-28
Yehova Amasamalira Anthu Ake
Yehova ndi wowolowa manja ndipo amatipatsa chakudya chambiri chauzimu.
‘Yehova wa makamu adzakonzera anthu a mitundu yonse phwando’
Kale, kudyera limodzi chakudya kunkasonyeza kuti anthuwo ndi ogwirizana komanso okondana
“La zakudya zabwinozabwino zokhala ndi mafuta a m’mafupa, ndiponso la vinyo wokoma kwambiri, wosefedwa bwino”
Zakudya zabwinozabwino ndiponso vinyo wokoma kwambiri komanso wosefedwa bwino zikuimira chakudya chauzimu chabwino kwambiri chimene Yehova amatipatsa