CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LUKA 14-16
Fanizo la Mwana Wolowerera
Mfundo zina zimene tikuphunzira mufanizoli
Ndi nzeru kukhalabe m’gulu la anthu a Mulungu lomwe ndi lotetezeka kwambiri komanso limene Yehova amaligwiritsa ntchito potisamalira mwachikondi
Ngati tayamba kuchoka panjira ya Mulungu tiyenera kudzichepetsa n’kubwerera kwa Yehova yemwe ndi wokonzeka kutikhululukira
Tiyenera kutengera chitsanzo cha Yehova pokhululukira komanso kulandira ndi manja awiri anthu amene abwerera mumpingo