Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb19 January tsamba 2
  • “Chifuniro cha Yehova Chichitike”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Chifuniro cha Yehova Chichitike”
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
  • Nkhani Yofanana
  • Muzisonyeza Kuti Mumaona Moyo Mmene Yehova Amauonera
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Anaimbidwa Mlandu Wosokoneza Anthu Komanso Kuukira Boma
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
  • “Chipulumutso Chanu Chikuyandikira”
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Paulo Anapempha Kukaonekera kwa Kaisara Ndipo Kenako Analalikira Mfumu Herode Agiripa
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
mwb19 January tsamba 2

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 21-22

“Chifuniro cha Yehova Chichitike”

21:8-14

Paulo ankaona kuti mzimu woyera unkamutsogolera kuti apite ku Yerusalemu komwe ankayembekezera kukakumana ndi mavuto. (Mac. 20:22, 23) Choncho pamene Akhristu ena omufunira zabwino ankamupempha kuti asapite, iye anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukulira ndi kunditayitsa mtima?” (Mac. 21:13) Ifenso sitiyenera kumafooketsa anthu amene akufuna kuchita zambiri potumikira Yehova.

Kodi tingalimbikitse bwanji Akhristu anzathu, m’malo mowafoola, pazochitika zotsatirazi?

  • M’bale akutsuka mawindo

    M’bale kapena mlongo wasankha kumagwira ntchito ya malipiro ochepa kuti azipeza nthawi yokwanira yochita utumiki

  • Banja likulalikira m’malo opezeka anthu ambiri m’dziko lina

    M’bale kapena mlongo akufuna kusamukira mumpingo wina womwe ukufunika ofalitsa ambiri

  • M’bale wosaona ali mu utumiki ndi mkazi wake

    M’bale kapena mlongo amayesetsa kulalikira ngakhale kuti amadwaladwala

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena