CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Kodi Mungatani Kuti Yehova Azikudalitsani?
Musamalambire milungu yopanda pake (Le 26:1; w08 4/15 4 ¶8)
Muzilambira Yehova m’njira imene amavomereza (Le 26:2; it-1 223 ¶3)
Muzimvera malamulo ake (Le 26:3, 12; w91 3/1 17 ¶10)
Aisiraeli amene ankayesetsa kumvera malamulo a Yehova, ankakhala naye pa mtendere komanso ankapeza madalitso ambiri.
Pa zinthu zotsatirazi, ndi ziti zimene mukusangalala nazo chifukwa chodalitsidwa ndi Yehova?
Kudziwa choonadi cha m’Baibulo
Kukhala ndi mtendere wamumtima
Kukhala ndi banja losangalala
Kukhala ndi chiyembekezo chabwino