Baibulo Ndi Buku la Maulosi Olondola Gawo 4
Baibulo Linalosera Kuti Khristu Adzazunzidwa Kenako N’kuphedwa
Nkhani zokwanira 8 zimene zikhale zikutuluka mu Galamukani!, zizifotokoza maulosi osiyanasiyana a m’Baibulo. Nkhanizi zikuthandizani kupeza mayankho a mafunso awa: Kodi maulosi a m’Baibulo analembedwa ndi anthu kapena pali umboni wakuti analembedwa ndi Mulungu? Kuwerenga nkhanizi kukuthandizani kudziwa zoona zenizeni.
PANTHAWI imene Yesu Khristu anali padziko lapansi, zaka 2,000 zapitazo, ankadziwa kuti adani ake adzamuzunza kenako n’kumupha. Iye ankadziwa zimenezi chifukwa chakuti anawerenga maulosi onena zimene zidzamuchitikire m’Malemba Achiheberi omwe ena amati Chipangano Chakale. Ena mwa maulosi amenewo analembedwa ndi mneneri Yesaya, kutatsala zaka 700 kuti Yesu abadwe. Kodi timadziwa bwanji kuti Yesaya analemba maulosi amenewa Yesu asanabadwe?
M’chaka cha 1947, m’busa wina wa mtundu wa Bedouin ku West Bank, anapeza mipukutu m’phanga lina m’dera la Qumran. Derali lili kumpoto chakum’madzulo kwa Nyanja Yakufa. Mipukutu imeneyi komanso ina imene anaipeza m’derali anayamba kuitchula kuti mipukutu ya ku nyanja yakufa. Pa mipukutuyi panali buku lonse la Yesaya.a Akatswiri amanena kuti bukuli ndi la m’zaka za m’ma 100 B.C.E., Yesu asanabadwe. Zimenezi zikusonyeza kuti Yesaya analemba zinthuzi zisanachitike. Kodi iye analosera chiyani za mavuto amene Khristu kapena kuti Mesiya adzakumane nawo?b Tiyeni tione awiri mwa maulosi amene Yesaya analosera.
Baibulo Linalosera Kuti Khristu Adzazunzidwa
Ulosi woyamba: “Msana wanga ndinaupereka kwa ondimenya.”—Yesaya 50:6.c
Kukwaniritsidwa kwake: M’chaka cha 33 C.E., Ayuda omwe anali adani ake a Yesu anamupititsa kwa bwanamkubwa wachiroma, dzina lake Pontiyo Pilato kuti akamuzenge mlandu. Koma Pilato anafuna kuti amumasule chifukwa sanamupeze ndi mlandu uliwonse. Komabe chifukwa choti Ayuda anakakamira kuti Yesu aphedwe, Pilato “anapereka chiweruzo chokwaniritsa zofuna za anthuwo,” ndipo anam’pereka kuti apachikidwe. (Luka 23:13-24) Koma asanachite zimenezi, “Pilato anatenga Yesu ndi kumukwapula.” Mawu amenewa angatanthauzenso kuti Pilato analamula kuti Yesu akwapulidwe. (Yohane 19:1) Choncho mogwirizana ndi zimene Yesaya analosera, Yesu sanakane koma ‘anapereka msana wake kwa omumenya.’
Zimene mbiri imasonyeza:
● Pali umboni wosonyeza kuti Aroma ankakonda kukwapula anthu asanawaphe. Mwachitsanzo buku lina linanena kuti: “Ankakwapula ndi chikwapu chokhala ndi tizingwe tachikopa tomwe kunsonga kwake ankamangirira tizitsulo takuthwa. Anthuwo . . . ankawavula malaya n’kumawamenya kumsana . . . mpaka msana wonse ukhale mabala okhaokha. Nthawi zina munthu ankatha kufa chifukwa chomenyedwa.” Koma Yesu sanafe chifukwa cha kumenyedwaku.
Baibulo Linalosera Kuti Khristu Adzaphedwa
Ulosi wachiwiri: “Anakhuthula moyo wake mu imfa.” (Yesaya 53:12)d Kuwonjezera pamenepa, lemba la Salimo 22:16 limati: “Andiboola m’manja anga ndi m’mapazi anga.”—Buku Lopatulika Ndilo Mau A Mulungu.
Kukwaniritsidwa kwake: Lemba la Maliko 15:15 limanena kuti: “[Pilato] atalamula kuti Yesu amukwapule, anamupereka kuti akamupachike.” Yesu anaphedwa mwankhanza kwambiri chifukwa anamukhomerera manja ndi mapazi pamtengo ndi misomali. (Yohane 20:25) Patatha maola angapo, “Yesu anafuula mokweza mawu, ndipo anatsirizika.”—Maliko 15:37.
Zimene mbiri imasonyeza:
● Pali mabuku ochepa a mbiri yakale, omwe amafotokoza mmene Yesu anaphedwera. Komabe katswiri wina wa mbiri yakale, dzina lake Tasitasi, yemwe anabadwa cha mu 55 C.E, analemba kuti: “Khristu yemwe [Akhristu] anatengera dzina lake, anazunzidwa mpaka imfa pa nthawi ya ulamuliro wa Tiberiyo, movomerezedwa ndi Pontiyo Pilato, mmodzi wa abwanamkubwa athu.”e Mawu a Tasitasiwa akugwirizana ndi nkhani za m’Mauthenga Abwino zomwe zimatchula Tiberiyo Kaisara, Pontiyo Pilato ndi akuluakulu ena omwe ankalamulira nthawi imeneyo.—Luka 3:1; 23:1-33; Yohane 19:1-24.
Komanso mbiri imasonyeza kuti Aroma ankapachika akapolo ndiponso anthu amene ankawaona kuti ndi zigawenga. Nthawi zina m’malo mowakhomerera ndi misomali ankawamangirira pamtengo. Buku lina linanena kuti: “Ankakhomerera manja ndi mapazi ndi misomali ndipo akatero ankangomusiya kuti adzizunzika. Munthuyo ankamva ludzu komanso ululu woopsa.”
Monga tanenera kale, Yesu ankadziwiratu kuti adzafa imfa yotereyi. N’chifukwa chake atatsala pang’ono kuphedwa anauza ophunzira ake molimba mtima kuti: “Tsopano tikupita ku Yerusalemu. Kumeneku, Mwana wa munthu akaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi, ndipo akamuweruza kuti aphedwe. Akam’pereka kwa anthu a mitundu ina kuti am’chitire chipongwe, kum’kwapula ndi kum’pachika pamtengo, ndipo pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.” (Mateyu 20:18, 19) Koma ena amafunsa kuti, n’chifukwa chiyani Yesu ankayenera kufa? Chifukwa chimene Yesu anafera chimatikhudza tonsefe komanso chimatipatsa chiyembekezo.
“Anaphwanyidwa Chifukwa cha Zochimwa Zathu”
Chifukwa choti anthufe ndi opanda ungwiro, timalakwitsa zinthu ndipo Baibulo limanena kuti umenewo ndi uchimo. Uchimo tingauyerekezere ndi mchenga umene walowa mu injini ya galimoto. Pang’ono ndi pang’ono mchengawo umawononga injiniyo ndipo kenako imadzasiya kugwira ntchito. Mofanana ndi zimenezi, anthufe timakalamba, kudwala kenako timamwalira. N’chifukwa chake lemba la Aroma 6:23 limati: “Malipiro a uchimo ndi imfa.” Komabe imfa ya Yesu inathandiza kuti timasuke ku uchimo ndi imfa. Kodi zimenezi zinatheka bwanji? Ulosi wina womwe Yesaya analemba, wonena za Khristu umati iye adzaphedwa, “chifukwa cha zolakwa zathu,” kapena ‘adzaphwanyidwa chifukwa cha zochimwa zathu,’ ndiponso kuti “chifukwa cha zilonda zake ifeyo tachiritsidwa.”f—Yesaya 53:5.
Ulosi wa Yesaya umatikumbutsa zimene Yesu ananena pa Yohane 3:16. Palembali iye anati: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”
Kuti muzikhulupirira Yesu, muyenera kuphunzira za iye. Nthawi ina popemphera Yesu ananena kuti: “Moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.” (Yohane 17:3) Baibulo ndi limene lingakuthandizeni kudziwa bwino Mulungu ndi Yesu.—2 Timoteyo 3:16.
Yesu akufuna kuti anthu ambiri adzapeze moyo wosatha. N’chifukwa chake atatsala pang’ono kufa, analosera kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse.” (Mateyu 24:14) M’magazini otsatira mudzakhala nkhani ziwiri zonena za maulosi zomwe zidzatithandize kuona kuti kulalikidwa kwa uthenga wabwino unali ulosi wolondola kwambiri.
[Mawu a M’munsi]
a Pali mpukutu umodzi wokha womwe uli ndi buku lonse la Yesaya. Mipukutu inayo ili ndi tizidutswa chabe ta bukuli.
b Werengani Galamukani! ya July 2012, kuti mudziwe maulosi ena a m’Baibulo onena za Mesiya.
c Mawu akuti “wanga” mu ulosi umenewu akunena za Khristu. Mwachitsanzo vesi 8 limanena kuti: “Amene [Mulungu] adzanene kuti ndine [Yesu Khristu] wolungama ali pafupi.” Yesu ali padziko lapansi anali munthu yekhayo amene Mulungu ankamuona kuti anali wolungama kapena kuti wopanda uchimo.—Aroma 3:23; 1 Petulo 2:21, 22.
d Lemba la Yesaya 52:13-15 ndi la Yesaya 53:1-12 lili ndi maulosi ena onena za Mesiya. Mwachitsanzo, pa Yesaya 53:7 pamati: “Anatengedwa ngati nkhosa yopita kokaphedwa . . . sanatsegule pakamwa pake.” Ndipo vesi 10 limanena kuti anapereka moyo wake “monga nsembe ya kupalamula.”
e Palinso anthu ena olemba mabuku akale omwe amanena za Khristu. Ena mwa anthuwa ndi Sutoniyasi, (anakhala m’nthawi ya atumwi), Pliny Wamng’ono yemwe anali bwanamkubwa wa ku Bituniya (anakhala ndi moyo chakumayambiriro kwa 100 C.E) ndi wolemba mbiri yakale dzina lake Josephus, (anakhala m’nthawi ya atumwi) yemwe ananena za “Yakobo, m’bale wake wa Yesu yemwe ankatchedwanso Khristu.”
f Yesu “sanachite tchimo” ndipo chifukwa cha zimenezi sankayenera kufa. (1 Petulo 2:22) Komabe anapereka moyo wake kuti atipulumutse ku uchimo ndi imfa. N’chifukwa chake imfa ya Yesu imatchedwa nsembe ya “dipo.” (Mateyu 20:28) Kuti mudziwe zambiri pa nkhaniyi, werengani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lomwenso limapezeka pa Webusaiti ya www.jw.org.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 20]
NSEMBE ZA NYAMA ZINKAIMIRA NSEMBE YA YESU
Chilamulo chimene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli chinali ndi malamulo amene ankaimira zimene Mesiya adzachite mtsogolo. Mwachitsanzo, Mwisiraeli akachimwa kapena akakhala kuti sanamvere Mulungu, ankayenera kupereka nsembe ya nyama yopanda chilema. (Levitiko 17:11; 22:21) Koma kodi nsembe zimenezi zinkachotseratu machimo a anthu? Ayi. (Aheberi 10:4) M’malomwake nsembezo zinkaimira nsembe imene idzachotseretu machimo onse. Baibulo limanena kuti nsembe imeneyi ndi, “Mwanawankhosa wa Mulungu amene akuchotsa uchimo wa dziko.” (Yohane 1:29; Aheberi 10:1, 5-10) Aliyense amene amakhulupirira nsembe ya Yesu Khristu ali ndi mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha.—Yohane 6:40.