Pindulani ndi Sukulu Yautumiki Wateokratiki ya 1996—Mbali 3
1 Mtumwi Paulo anafuna kuti abale ake ampempherere kuti apeze luso la kulankhula uthenga wabwino molimbika. (Aef. 6:18-20) Timafuna kukulitsa luso limodzimodzilo. Ndi cholinga chimenecho, timayamikira thandizo limene Sukulu Yautumiki Wateokratiki imapereka, mmene ofikapo oyenerera amalimbikitsidwa kulembetsa.
2 Monga ophunzira, timalandira uphungu wa munthu aliyense payekha wotithandiza kuwongolera kalankhulidwe kathu ndi maluso a kuphunzitsa. (Miy. 9:9) Tingapindulenso mwa kumvetsera uphungu umene ophunzira ena amalandira, kugwiritsira ntchito zimene timaphunzira pa ife eni. Pokonzekera nkhani, tiyenera kuphunzira magwero a nkhani mosamalitsa kuti titsimikizire kuti malongosoledwe athu pankhaniyo ngolondola. Mfundo zazikulu ndi malemba amene tidzagwiritsira ntchito ziyenera kugwirizana ndi nkhani yonse. Ngati nkhaniyo ikuphatikizapo munthu wina, iyenera kuyesezedwa bwino pakali nthaŵi sukuluyo isanafike. Pamene tipanga kupita patsogolo, tiyenera kuyesayesa kulankhula mwachibadwa, tikumagwiritsira ntchito manotsi m’malo moŵerenga zolemba.
3 Onse amene amapatsidwa nkhani m’sukulu ayenera kufika msanga, kupereka silipi lawo la Uphungu wa Kulankhula kwa woyang’anira sukulu, ndi kukhala kutsogolo kwa holo. Alongo ayenera kudziŵitsa woyang’anira sukulu za mkhalidwe wa nkhani yawo pasadakhale kuti kaya adzaimirira kapena adzakhala pansi. Kugwirizanika m’njira zimenezi kumachirikiza kayendedwe kamyaa ka programu ndipo kumathandiza aja amene amasamalira ku pulatifomu kulinganiza zonse pasadakhale.
4 Kukonzekera Nkhani Na. 2: Chifuno chimodzi cha kuŵerenga Baibulo nchakuthandiza wophunzira kuwongolera luso lake la kuŵerenga. Kodi zimenezi zingachitidwe bwino kwambiri motani? Kuŵerenga nkhaniyo momveketsa mawu mobwerezabwereza ndiko njira yabwino koposa yochitira zimenezo, ndipo wophunzira angaloŵetse mfundo zazikulu m’maganizo. Dziŵani matchulidwe a mawu m’vesi. Ndiyeno yesezani kupereka nkhaniyo momveketsa mawu kuti muzoloŵere njira ya kafotokozedwe ka wolemba wake. Oŵerenga ena amapeza kuti kuyeseza kuŵerenga momveketsa mawu ataima pakalilole kumawathandiza kuwongolera kuyang’ana omvetsera.
5 Kuŵerenga Baibulo nkofunika kwambiri kwa achichepere ndi achikulire omwe. Kaŵirikaŵiri pamakhala mikhalidwe imene imafunikiritsa kuŵerenga Baibulo momveketsa mawu. Imeneyi ndiyo nkhani ina ya Sukulu Yautumiki Wateokratiki. Ndipo ife tonse timaŵerenga Malemba pamene tilankhula kwa anthu mu utumiki wathu. Koma kodi timawaŵerenga bwino? Kodi tawayeseza kuti tisakadodome, kuti tikagogomezere mawu amene ali ogwirizana ndi chigomeko chathu ndi kuti kuŵerenga kwathu kukhale kwachibadwa, kokambitsirana? Kukonzekera kumafunikadi pankhani ya kuŵerenga Baibulo. Kumbukirani kuti ameneŵa ndi Mawu a Mulungu, amene ali odzala ndi mawu apadera abwino kwambiri ndi osonkhezera mtima, ndiponso opereka malingaliro olondola ndi anzeru. Tiyenera kuyesayesa kuwafotokoza moyenera kaamba ka phindu la omvetsera. Ngati tidziŵa pasadakhale kuti tidzaŵerenga Baibulo, tiyenera kukonzekera mosamalitsa, kuti tipeŵe kudodoma pamawu achilendo, ziganizo kapena mafotokozedwe ake.
6 Makolo angathandize ana awo kukonzekera nkhani yoŵerenga. Zimenezi zingaphatikizepo kumvetsera pamene mwanayo akuyeseza ndiyeno kumpatsa malingaliro othandiza a kuwongolera. Nthaŵi yoperekedwa imaloleza munthu kunena mawu oyamba achidule ndi mapeto oyenera amene amasonyeza kugwira ntchito kwa mfundo zazikulu. Motero wophunzira amakulitsa luso lake la kulankhula mwachibadwa.
7 Wamasalmo anapempha mwapemphero kuti: “Ambuye, tsegulani pamilomo yanga; ndipo pakamwa panga padzalalikira ulemekezo wanu.” (Sal. 51:15) Kukhala ndi phande kwathu mu Sukulu Yautumiki Wateokratiki kutithandizetu kukhutiritsa chikhumbo chimodzimodzichi.