Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/96 tsamba 2
  • Misonkhano Yautumiki ya March

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Misonkhano Yautumiki ya March
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira March 4
  • Mlungu Woyambira March 11
  • Mlungu Woyambira March 18
  • Mlungu Woyambira March 25
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 3/96 tsamba 2

Misonkhano Yautumiki ya March

Mlungu Woyambira March 4

Nyimbo Na. 1

Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Mbiri Yateokrase.

Mph. 15: “Yamikani Yehova ‘Masiku Onse.’” Mafunso ndi mayankho. Ŵerengani ndime 2-5 ngati nthaŵi ilola. Perekani chilimbikitso chabwino cha kuchita ntchito ya upainiya wothandiza ndi wokhazikika.

Mph. 20: “Chidziŵitso Chonena za Mulungu Woona Chimatsogolera ku Moyo.” Fotokozani maulaliki osonyezedwawo. Sonyezani chitsanzo chimodzi kapena ziŵiri.

Nyimbo Na. 78 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira March 11

Nyimbo Na. 164

Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Lipoti la maakaunti.

Mph. 20: “Pindulani ndi Sukulu Yautumiki Wateokratiki ya 1996—Mbali 3.” Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira sukulu. Limbikitsani onse amene angathe, kulembetsa ndi kupereka nkhani zawo mokhulupirika.

Mph. 15: “Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa ‘Amithenga a Mtendere Waumulungu’ wa 1996.” Nkhani ya mafunso ndi mayankho ya mlembi.

Nyimbo Na. 211 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira March 18

Nyimbo Na. 6

Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Aja amene akuchititsa maphunziro ayenera kulimbikitsa atsopano amene akupita bwino patsogolo m’phunziro lawo la Baibulo kukalimira kukhala ofalitsa osabatizidwa. Makolo angathandizenso ana awo kukhala ofalitsa. Fotokozani njira yake yoyenera yolongosoledwa mu Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu, masamba 97-100.

Mph. 15: Fotokozani Mfundo Zazikulu za mu 1996 Yearbook of Jehovah’s Witnesses. Banja likambitsirana mbali zina zokondweretsa zonena za ntchito yathu yapadziko lonse zofotokozedwa pamasamba 3-5 ndi 33. Avomerezana kuti tsiku lililonse adzayesa kuŵerenga pamodzi masamba angapo a Yearbook pambuyo pa kukambitsirana lemba la Baibulo lolinganizidwa mu Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku.

Mph. 20: “Thandizani Ena Kupeza Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo.” Fotokozani maulaliki osonyezedwa kaamba ka maulendo obwereza. Phatikizanipo chitsanzo chimodzi kapena ziŵiri. Gogomezerani chonulirapo cha kuyambitsa maphunziro.

Nyimbo Na. 130 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira March 25

Nyimbo Na. 5

Mph. 15: Zilengezo zapamalopo. Pendani “Zikumbutso za Chikumbutso.” Fotokozani chifukwa chake kuli kofunika kufikapo. (Onani Nsanja ya Olonda ya February 15, 1985, masamba 16, 17.) Fotokozani za makonzedwe othandiza okalamba, athanzi lofooka, ndi atsopano kupezekapo. Longosolani za makonzedwe a ntchito yowonjezereka ya utumiki wakumunda mkati mwa mlungu ukudzawo. Ndiponso, kambani nkhani yakuti, “Kumene Amachereza Alendo,” patsamba 32 la Galamukani! wachingelezi wa September 22, 1995.

Mph. 15: Bokosi la Mafunso. Nkhani ya mkulu. Fotokozani zifukwa zimene zimatisonkhezera kukhala owoloŵa manja, monga momwe kwafotokozedwera mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 1992, masamba 16-17.

Mph. 20: “Kukonzekera—Mfungulo ya Chipambano.” Mafunso ndi mayankho. Tchulani kuti tidzagaŵira sabusikripishoni ya Nsanja ya Olonda ndi makope a magazini mu April ndi May. Pangani makonzedwe ake tsopano lino mwa kupeza masilipi a sabusikripishoni osalembedwa ndi kulinganiza kudzachirikiza makonzedwe ampingo a ntchito ya magazini. Gogomezerani mfundo yakuti April ndi May iyenera kukhala miyezi yapadera ya mkupiti wamagazini.

Nyimbo Na. 7 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena