Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/13 tsamba 3-6
  • Kodi Tingawathandize Bwanji?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Tingawathandize Bwanji?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Nkhani Yofanana
  • Gwiritsani Ntchito Kabuku Kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Njira Ina Imene Tingagwiritsire Ntchito Kabuku ka Kodi Baibulo Lili ndi Uthenga Wotani?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Kabuku Katsopano Kamene Tidzagawira
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
  • Gwiritsirani Ntchito Mabrosha Osiyanasiyana Mu Utumiki Wanu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
km 12/13 tsamba 3-6

Kodi Tingawathandize Bwanji?

1. Kodi n’zotheka kuyamba kuphunzira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndi aliyense tisanakambirane naye mfundo za m’mabuku ena? Fotokozani.

1 Kuti munthu akhale mtumiki wa Yehova, amafunika kuphunzira zimene Baibulo limaphunzitsa. Komabe anthu ena sali m’zipembedzo zachikhristu ndipo saona kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu. Ena sakhulupirira n’komwe zoti kuli Mulungu ndipo saona kuti Baibulo ndi buku lapadera. Kwa anthu oterewa zingakhale zovuta kuyamba kuphunzira nawo buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Ndiye kodi tingagwiritse ntchito mabuku ati kuti tithandize anthu amenewa, tisanayambe kuphunzira nawo buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani? Taonani mfundo zotsatirazi zimene abale ndi alongo ochokera m’mayiko 20 ananena pa nkhaniyi.

2. Munthu akatiuza kuti sakhulupirira zoti kuli Mulungu, kodi tifunika kudziwa chiyani ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika?

2 Anthu Amene Sakhulupirira Zoti Kuli Mulungu: Munthu wina akakuuzani kuti sakhulupirira zoti kuli Mulungu, zimakhala bwino kudziwa chifukwa chake. Kodi n’chifukwa choti amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina? Kodi anasiya kukhulupirira Mulungu chifukwa cha zinthu zopanda chilungamo zimene zikuchitika m’dzikoli kapena chifukwa choona kuti zipembedzo zimachita zinthu zachinyengo? Kodi anachokera m’dziko limene limaletsa anthu kukhulupirira Mulungu? Mwina sakhulupirira Mulungu chifukwa choti sanaganizepo n’komwe ngati kukhulupirira Mulungu kuli ndi phindu lililonse. Abale ndi alongo ambiri apeza kuti kufunsa munthuyo kuti, “Kodi mwakhala mukukhulupirira zimenezi kwa nthawi yaitali bwanji?” kumachititsa kuti munthuyo afotokoze maganizo ake. Munthuyo akamafotokoza, mvetserani ndipo musamudule mawu. Tikadziwa chifukwa chimene munthuyo sakhulupirira Mulungu, tingadziwe zoyenera kumuyankha komanso buku lomwe tingam’patse.—Miy. 18:13.

3. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza munthu amene tikukambirana naye komanso zomwe amakhulupirira?

3 Mukamayankha, muzisamala kuti munthuyo asaone ngati mukutsutsana ndi maganizo ake. Wa Mboni wina wa ku America ananena kuti: “Kulemekeza ufulu wa anthu wosankha zimene akufuna kukhulupirira n’kofunika kwambiri. M’malo mokhala ndi cholinga chofuna kuwina mkangano, ndi bwino kufunsa mafunso amene angathandize munthuyo kuganiza komanso kupeza yekha yankho lolondola.” Woyang’anira dera wina amadikira munthu akamafotokoza maganizo ake ndipo kenako amayamba ndi kumufunsa kuti, “Koma kodi mukuganiza kuti mfundo zotsatirazi zingakhalenso zoona?”

4. Kodi tingathandize bwanji anthu a m’chipembedzo chachibuda?

4 Mfundo yoti kuli Mulungu ndi yachilendo kwa anthu ambiri a chipembedzo chachibuda. Abale ndi alongo ena a ku Britain akakumana ndi anthu oterewa, amakonda kugwiritsa ntchito kabuku kachingelezi kakuti Lasting Peace and Happiness—How to Find Them. Akamaliza kukambirana mawu oyamba, amapita mutu wakuti “Is There Really a Most High Creator?” ndipo kenako amakambirana mutu wakuti “A Guidebook for the Blessing of All Mankind.” Akatero amamusonyeza munthuyo buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, n’kumuuza kuti, “Ngakhale simukhulupirira zoti kuli Mulungu, kuphunzira Baibulo kukhoza kukuthandizani chifukwa lili ndi malangizo othandiza.” Mpainiya wina wa ku America amene amalalikira m’gawo la anthu olankhula Chitchainizi anati: “Anthu ambiri a m’gawo lathu amakonda kuwerenga moti tikawapatsa magazini kapena kabuku, tikamabwererakonso timapeza atamaliza kuwerenga. Komabe mfundo yoti munthu akhoza kumaphunzira Baibulo, ndi yachilendo kwa iwo. Choncho ndimakonda kuwasiyira kabuku koti Uthenga Wabwino pa ulendo woyamba chifukwa kabukuka kanalembedwa m’njira yolimbikitsa kukambirana.” Woyang’anira dera wina wa ku America amene amatumikira m’dera la anthu olankhula Chitchainizi ananena kuti n’zotheka kukambirana ndi munthu buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ngakhale pa ulendo woyamba. Koma ndi bwino kuyamba ndi kuphunzira mutu 2, umene umanena za Baibulo, kusiyana n’kuyamba ndi mutu 1, umene umanena za Mulungu.

5. N’chifukwa chiyani kuleza mtima n’kofunika?

5 Pamatenga nthawi kuti munthu ayambe kukhulupirira zoti kuli Mulungu, choncho kuleza mtima n’kofunika kwambiri. Nthawi zina, ngakhale titakambirana ndi munthu kwa maulendo angapo, munthuyo angakhale asanayambebe kukhulupirira zoti kuli Mulungu. Koma n’kutheka kuti patapita nthawi, akhoza kuyamba kuganiza kuti mwina kulidi Mulungu, apo ayi akhoza kumvetsa chifukwa chake anthu ena amanena kuti kuli Mulungu.

6. N’chifukwa chiyani anthu ena sachita chidwi ndi Baibulo?

6 Anthu Amene Sakhulupirira Kuti Baibulo Ndi Lothandiza: Palinso anthu ena amene amakhulupirira kuti kuli Mulungu koma alibe chidwi ndi zimene Baibulo limaphunzitsa chifukwa sakhulupirira kuti Baibulo ndi mawu a Mulungu. Mwina amakhala m’dziko limene kulibe Chikhristu ndipo amaona kuti Baibulo ndi buku lokhudza Matchalitchi Achikhristu okha basi. Kapena amakhala m’dziko limene limati ndi lachikhristu koma anthu ake satsatira mfundo za m’Baibulo ndipo angamaone kuti Baibulo ndi losathandiza kwa iwowo. Kodi tingathandize bwanji anthu oterewa kuti ayambe kuchita chidwi ndi Baibulo ndipo kenako adzavomere kuphunzira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani?

7. Kodi nthawi zambiri njira yabwino yothandizira anthu kuchita chidwi ndi Baibulo ndi iti?

7 Ofesi ya nthambi ya ku Greece inanena kuti: “Njira yabwino yothandizira anthu amene amaona ngati Baibulo ndi losathandiza, ndi kuwerenga nawo m’Baibulolo kuti aone zimene limanena.” Abale ndi alongo ambiri apeza kuti uthenga wa m’Baibulo umakhudza kwambiri mtima wa munthu kuposa zilizonse zimene iwo anganene. (Aheb. 4:12) Kuona dzina la Mulungu m’Baibulo kwathandiza anthu ena kukhala ndi chidwi chofuna kudziwa zimene zili m’Baibulo.” Ofesi ya nthambi ku India inalemba kuti: “Ahindu ambiri amachita chidwi akadziwa zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani ya zimene zimachitika munthu akamwalira. Nkhani inanso imene amachita nayo chidwi ndi ya zimene Baibulo limanena zokhudza dziko latsopano limene simudzakhala tsankho.” Nthawi zambiri kutchula mavuto amene anthu a m’deralo akukumana nawo kumathandiza kuti abale ndi alongo apeze mpata wosonyeza anthuwo zimene Ufumu wa Mulungu udzachite pothetsa mavuto amenewo.

8. Kodi tingawauze chiyani anthu amene sakonda Baibulo chifukwa cha zimene Matchalitchi Achikhristu amanena?

8 Ngati munthu wina sakonda Baibulo chifukwa cha zimene Matchalitchi Achikhristu amachita, ndi bwino kumuuza kuti Matchalitchi Achikhristu amapotoza zimene Baibulo limanena. Ofesi ya nthambi ya ku India inanena kuti: “Nthawi zambiri pamafunika kuwathandiza anthu kuti adziwe zoti matchalitchi satsatira zimene Baibulo limanena.” Ofesi ya nthambiyi inanenanso kuti nthawi zambiri Ahindu amachita chidwi ndi mutu 4 wa m’kabuku kakuti Kodi Chifuno cha Moyo N’chiyani? Kodi Mungachipeze Motani? kamene kamafotokoza zimene matchalitchi achita pofuna kupotoza komanso kuwononga Mawu a Mulungu. Mpainiya wina wa ku Brazil amauza anthu kuti: “Mungachite bwino kuphunzira Baibulo kuti mudziwe zimene limanena. Anthu ambiri amachita zimenezi popanda kuligwirizanitsa ndi zimene matchalitchi amanena. Mungadabwe kwambiri ndi zimene mungaphunzire.”

9. N’chifukwa chiyani sitiyenera kugwa mphwayi tikapeza munthu amene akusonyeza kuti alibe chidwi chofuna kudziwa zomwe Baibulo limaphunzitsa?

9 Mulungu amaona mtima wa munthu aliyense. (1 Sam. 16:7; Miy. 21:2) Amakoka anthu a mtima wabwino kuti ayambe kumulambira. (Yoh. 6:44) Ambiri mwa anthu amenewa amakhala oti poyamba sankadziwa Mulungu kapenanso sankadziwa zambiri zokhudza Baibulo. Ntchito yathu yolalikira imawapatsa mwayi woti “apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.” (1 Tim. 2:4) Choncho ngati mwapeza munthu amene akusonyeza kuti alibe chidwi chofuna kudziwa zomwe Baibulo limaphunzitsa, musagwe mphwayi. Yesetsani kugwiritsa ntchito buku limene lingamuthandize kukhala ndi chidwi ndi Baibulo. Pakapita nthawi mungathe kudzasintha n’kuyamba kuphunzira naye buku limene timaphunzitsira anthu Baibulo lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?

[Bokosi patsamba 4]

Munthu akanena kuti sakhulupirira zoti kuli Mulungu, mungachite zotsatirazi:

• Mufunseni kuti: “Kodi mwakhala mukukhulupirira zimenezi kwa nthawi yaitali bwanji?” Zimenezi zingakuthandizeni kuti mudziwe chifukwa chake sakhulupirira Mulungu.

• Ngati munthuyo ndi wachipembedzo chachibuda, mungagwiritse ntchito kabuku kakuti, Lasting Peace and Happiness—How to Find Them, tsamba 9 mpaka 12.

• Ngati amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina, mungagwiritse ntchito zinthu zotsatirazi:

Nkhani za mu Galamukani! za mutu wakuti “Kodi Zinangochitika Zokha?” zomwe poyamba zinkakhala ndi mutu wakuti “Panagona Luso!”

Vidiyo yakuti, The Wonders of Creation Reveal God’s Glory

Timabuku takuti Moyo Wokhutiritsa Mmene Mungaupezere, mutu 4; Was Life Created?; ndi kakuti The Origin of Life—Five Questions Worth Asking

• Ngati anasiya kukhulupirira Mulungu chifukwa cha zinthu zopanda chilungamo komanso mavuto ena amene amachitika padzikoli, mabuku otsatirawa angamuthandize:

Buku lakuti, Is There a Creator Who Cares About You?, mutu 10

Kabuku kakuti, Kodi Mulungu Amatisamaliradi? chigawo 6 ndi kakuti, Kodi Chifuno cha Moyo N’chiyani? mutu 6

• Akangoyamba kuvomereza mfundo yoti kuli Mulungu, yambani kuphunzira naye buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Zingakhale bwino kuyambira mutu 2 kapena mutu wina umene ungagwirizane ndi munthuyo.

[Bokosi patsamba 5]

Ngati munthuyo sakhulupirira Baibulo, mungachite zotsatirazi:

• Phunzirani naye mutu 17 ndi 18 m’buku lakuti, Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation?

• Ngati munthuyo ndi wachipembedzo chachihindu, gwiritsani ntchito kabuku kakuti, Why Should We Worship God in Love and Truth?

• Ngati ndi wachipembedzo chachiyuda, mungagwiritse ntchito kabuku kakuti, Will There Ever Be a World Without War? tsamba 3 mpaka 11.

• Kambiranani naye phindu limene munthu amapeza akamatsatira mfundo za m’Baibulo. Mungagwiritse ntchito mabuku otsatirawa pofuna kumusonyeza kuti kutsatira mfundo za m’Baibulo n’kothandiza:

Nkhani za mu Galamukani! za mutu wakuti, “Mfundo Zothandiza Mabanja”

Vidiyo yakuti, The Bible—Its Power in Your Life

Kabuku kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu, phunziro 9 ndi 11; Buku la Anthu Onse, tsamba 22 mpaka 26; ndi kakuti Moyo Wokhutiritsa Mmene Mungaupezere, mutu 2

Ngati munthuyo ali wachipembedzo chachibuda, mungagwiritse ntchito kabuku kakuti, The Pathway to Peace and Happiness, tsamba 3 mpaka 7.

Ngati ndi Msilamu, gwiritsani ntchito kabuku kakuti, Real Faith—Your Key to a Happy Life, mutu 3.

Ngati mukulalikira m’dera limene anthu amadana ndi Baibulo, zingakhale bwino pa ulendo woyamba osanena kuti uthenga umene mukulalikira ndi wochokera m’Baibulo mpaka mutacheza ndi munthuyo maulendo angapo.

• Fotokozani mmene ulosi wa m’Baibulo umakwaniritsidwira. Mungagwiritse ntchito zinthu zotsatirazi:

Vidiyo yakuti, The Bible—Accurate History, Reliable Prophecy

Kabuku kakuti, Buku la Anthu Onse, tsamba 27 mpaka 29

• Munthuyo akayamba kufunsa zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani zosiyanasiyana, yambani kuphunzira naye buku lakuti, Baibulo Limaphunzitsa Chiyani.

[Bokosi patsamba 6]

Ngati munthu wanena kuti, “Sindikhulupirira Mulungu” munganene kuti:

• “Kodi ndingakufotokozereni mwachidule zimene zinandichititsa ineyo kuti ndiyambe kukhulupirira kuti kuli Mlengi?” Ndiyeno kambiranani naye mfundo zimene zili patsamba 74 mpaka 76 m’buku la Kukambitsirana kapena muuzeni kuti mudzamubweretsera buku kapena kanthu kena kamene kali ndi nkhani yomwe inuyo inakusangalatsani kwambiri.

• “Koma zikanakhala kuti Mulungu alipo, kodi inuyo mukanakonda kuti akhale wotani?” Anthu ambiri amayankha kuti akanakonda Mulunguyo akanakhala wachikondi, chilungamo, chifundo komanso wopanda tsankho. Ndiyeno muonetseni kuchokera m’Baibulo kuti Mulungu ali ndi makhalidwe amenewa. (Mungathenso kugwiritsa ntchito mutu 1 m’buku lakuti, Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kuyambira pandime 6.)

Ngati munthu wanena kuti “Sindikhulupirira Baibulo” munganene kuti:

• “Pali anthu ambiri amenenso sakhulupirira Baibulo. Ena amati salikhulupirira chifukwa siligwirizana ndi sayansi kapena chifukwa choti mfundo zake n’zosathandiza. Kodi inuyo munayamba mwawerengapo Baibulo? [Yembekezerani ayankhe. Ndiyeno muonetseni mawu oyamba patsamba 3 m’kabuku kakuti Buku la Anthu Onse ndipo musiireni kabukuko.] Anthu ena amaona kuti Baibulo ndi buku losathandiza chifukwa zipembedzo zimamasulira molakwa zimene Baibulo limaphunzitsa. Ndikadzabweranso tidzakambirana tsamba 4 ndi 5 kuti ndidzakusonyezeni chitsanzo cha zimenezi.”

• “Anthu ambiri amaganizanso choncho. Koma kodi ndingakuonetseni mfundo ina imene inandichititsa kuti ndizikhulupirira Baibulo? [Werengani lemba la Yobu 26:7 kapena Yesaya 40:22, lomwe limasonyeza kuti Baibulo ndi lolondola pa nkhani za sayansi.] M’Baibulo mulinso malangizo anzeru othandiza mabanja. Ndikadzabweranso ndidzakusonyezani chitsanzo cha malangizo oterewa.”

• “Zikomo kwambiri pondiuza maganizo anu. Komano zikanakhala kuti Mulungu analemba buku loti anthu aziwerenga, kodi mukuganiza kuti bukulo likanakhala ndi nkhani zotani?” Kenako musonyezeni vesi limene likugwirizana ndi zimene wanenazo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena