CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 21-22
“Chifuniro cha Yehova Chichitike”
Paulo ankaona kuti mzimu woyera unkamutsogolera kuti apite ku Yerusalemu komwe ankayembekezera kukakumana ndi mavuto. (Mac. 20:22, 23) Choncho pamene Akhristu ena omufunira zabwino ankamupempha kuti asapite, iye anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukulira ndi kunditayitsa mtima?” (Mac. 21:13) Ifenso sitiyenera kumafooketsa anthu amene akufuna kuchita zambiri potumikira Yehova.