“Muzichita Zimenezi” Chikumbutso Chidzachitika pa April 5
1. N’chifukwa chiyani mwambo wa Chikumbutso uli wofunika kwambiri?
1 “Muzichita zimenezi pondikumbukira.” (Luka 22:19) Ponena mawu amenewa, Yesu anali kulamula otsatira ake kuti azikumbukira imfa yake monga nsembe yowombola anthu. Chifukwa cha zimene dipo linakwaniritsa, palibe tsiku limene lingakhale lofunika kapena la mtengo wapatali kwambiri kwa Akhristu pa chaka, kuposa tsiku la Chikumbutso. Pamene tsiku la Chikumbutso la chaka chino la April 5 likuyandikira, kodi tingamuyamikire bwanji Yehova?—Akol. 3:15.
2. Kodi kuphunzira ndiponso kusinkhasinkha kungatithandize bwanji kuyamikira Chikumbutso?
2 Konzekerani: Nthawi zonse timakonzekera zinthu zimene timaziona kuti n’zofunika. Tikhoza kukonzekera Chikumbutso pokonzekeretsa mitima yathu mwa kuphunzira ndiponso kusinkhasinkha monga banja zinthu zimene zinachitika masiku omalizira a moyo wa Yesu padziko lapansi. (Ezara 7:10) Malemba ena amene tingawerenge pa nthawiyi ali pakalendala ndi m’kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku. Mungapezenso ndandanda ya zimene zinachitika ndiponso machaputala ake mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 2011, masamba 23 ndi 24, zochokera m’buku la Munthu Wamkulu.
3. Kodi kuwonjezera zochita mu utumiki kungasonyeze bwanji kuti timayamikira Chikumbutso?
3 Muzilalikira: Tikhozanso kusonyeza kuyamikira ngati titagwira nawo ntchito yolalikira ndi mtima wathu wonse. (Luka 6:45) Ntchito ya padziko lonse yoitanira anthu ku Chikumbutso idzayamba Loweruka pa March 17. Kodi mungasinthe zina ndi zina pa moyo wanu kuti mudzathere nthawi yambiri mu utumiki kapenanso kuchita upainiya wothandiza? Bwanji osakambirana ndi anthu a m’banja lanu za nkhani imeneyi pa nthawi ya Kulambira kwa Pabanja?
4. Kodi tingapeze phindu lotani chifukwa chopezeka pa Chikumbutso?
4 Tikamapezeka pa Chikumbutso chaka ndi chaka timapindula kwambiri. Tikamaganizira za kuwolowa manja kwa Yehova popereka mwana wake wobadwa yekha monga dipo, timakhala osangalala ndiponso timakonda kwambiri Mulungu. (Yoh. 3:16; 1 Yoh. 4:9, 10) Zimenezi zimatichititsa kuti tisamakhale moyo wongodzisangalatsa. (2 Akor. 5:14, 15) Zimatilimbikitsanso kukhala ndi mtima wotamanda Yehova kwa anthu onse. (Sal. 102:19-21) Choncho, atumiki a Yehova amene amayamikira dipoli akuyembekezera mwachidwi mwayi ‘wolengeza imfa ya Ambuye’ umene tikhale nawo pa nthawi ya Chikumbutso pa April 5.—1 Akor. 11:26.