Bokosi la Mafunso
◼ Kodi N’chiyani Chingatichititse Kusiya Kuphunzira Baibulo ndi Munthu?
Ngati munthu sakusintha ngakhale kuti taphunzira naye kwa nthawi yaitali, tiyenera kumusiya koma tizichita zimenezi mosamala. (Mat. 10:11) Tiyenera kudzifunsa kuti: Kodi tikapangana tsiku loti tiphunzire naye amapezeka? Kodi amakonzekereratu phunzirolo? Kodi anafikapo ku misonkhano ya mpingo? Kodi amauza anzake zimene akuphunzirazo? Kodi akusintha moyo wake chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo? Poyankha mafunsowa, tiyenera kuganiziranso msinkhu wake komanso zimene angakwanitse kuchita chifukwa anthu sachita zinthu mofanana. Ngakhale titasiya kuphunzira naye, tiyenera kumuthandiza kudziwa kuti titha kudzapitiriza m’tsogolo ngati angafune.—1 Tim. 2:4.