Masalimo
Nyimbo.
98 IMBIRANI Yehova nyimbo yatsopano,+
Pakuti zimene wachita ndi zodabwitsa.+
Dzanja lake lamanja, ndithu mkono wake woyera, wabweretsa chipulumutso.+
2 Yehova wachititsa chipulumutso chake kudziwika.+
Chilungamo chake wachisonyeza ku mitundu ya anthu.+
3 Iye wakumbukira lonjezo lake losonyeza kukoma mtima kosatha ndi kukhulupirika kwake ku nyumba ya Isiraeli.+
Malekezero onse a dziko lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.+
4 Fuulirani Yehova mosangalala chifukwa wapambana, inu nonse anthu a padziko lapansi.+
Kondwerani, fuulani mosangalala ndi kuimba nyimbo zomutamanda.+
5 Imbirani Yehova nyimbo zomutamanda ndi zeze,+
Muimbireni nyimbo ndi zeze ndi kumutamanda ndi nyimbo zokoma.+
6 Fuulani mwa kuimba malipenga ndi mphalasa.*+
Fuulani mosangalala pamaso pa Mfumu Yehova, chifukwa wapambana.