9 Pambuyo pake, Abulamu anasamutsa hema wake kumeneko. Kuyambira pa nthawi imeneyi, iye ankangokhalira kumanga ndi kusamutsa msasa, kulowera ku Negebu.+
22 Atapita ku Negebu,+ anakafika ku Heburoni.+ Kumeneko anapezako Ahimani, Sesai ndi Talimai,+ mbadwa za Anaki.*+ Mzinda wa Heburoni+ unamangidwa zaka 7 mzinda wa Zowani+ wa ku Iguputo usanamangidwe.
7 Kenako anafika kumzinda wa mpanda wolimba wa Turo+ ndiponso kumizinda yonse ya Ahivi+ ndi Akanani. Pamapeto pake anafika ku Beere-seba+ ku Negebu,+ m’dziko la Yuda.
19 Iwo adzatenga dera la Negebu kukhala lawo, komanso adzatenga dera lamapiri la Esau,+ dera la Sefela ndi dera la Afilisiti.+ Iwo adzatenganso madera a Efuraimu+ ndi Samariya kukhala awo.+ Benjamini adzatenga dera la Giliyadi+ kukhala lake.