Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 31:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Koma bambo anu akhala akundipusitsa, ndipo asintha malipiro anga maulendo 10. Ngakhale ndi choncho, Mulungu sanawalole kuti andichite choipa.+

  • Deuteronomo 24:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Uzim’patsa malipiro ake+ tsiku lililonse, ndipo dzuwa lisalowe usanam’patse malipiro ake chifukwa iye ndi wovutika. Iye akuyembekezera malipiro akewo mwachidwi, ndipo angafuule kwa Yehova chifukwa cha zimene iweyo wam’chitira,+ iwe n’kupezeka kuti wachimwa.+

  • 1 Mafumu 5:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Tsopano lamulani kuti anthu andidulire mitengo ya mkungudza ya ku Lebanoni.+ Antchito anga adzakhala limodzi ndi antchito anu ndipo ndidzakupatsani malipiro a antchito anu malingana ndi zonse zomwe munganene. Inuyo mukudziwa bwino kuti pakati pathu palibenso anthu odziwa kudula mitengo ngati Asidoni.”+

  • Yobu 7:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 Monga kapolo, iye amakhala wefuwefu kufunafuna mthunzi,+

      Ndipo ngati munthu waganyu, amadikirira malipiro ake.+

  • Yeremiya 22:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 “Tsoka amene akumanga nyumba yake+ komanso zipinda zake zam’mwamba mopanda chilungamo mwa kugwiritsa ntchito anthu kwaulere, osawapatsa malipiro.+

  • 1 Timoteyo 5:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Pakuti lemba limati: “Usamange ng’ombe pakamwa pamene ikupuntha mbewu.”+ Komanso limati: “Wantchito ayenera kulandira malipiro ake.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena