Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 19:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Usabere mnzako mwachinyengo+ ndipo usafwambe aliyense.+ Malipiro a munthu waganyu asagone m’nyumba mwako kufikira m’mawa.+

  • Deuteronomo 24:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 “Usachitire chinyengo waganyu wovutika ndiponso wosauka n’kumubera, kaya akhale mmodzi wa abale ako kapena mmodzi mwa alendo okhala m’dziko lanu, amene ali m’mizinda yanu.+

  • Mika 3:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Inu mukumanga Ziyoni ndi ntchito zokhetsa magazi ndipo mukumanga Yerusalemu mwa kuchita zinthu zopanda chilungamo.+

  • Habakuku 2:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 “‘Tsoka kwa munthu amene akupezera nyumba yake phindu mwachinyengo.+ Iye akuchita zimenezi kuti amange chisa chake pamalo okwezeka ndi cholinga choti tsoka lisamupeze.+

  • Habakuku 2:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 “‘Tsoka kwa munthu amene akumanga mzinda mwa kukhetsa magazi, amenenso wakhazikitsa tauni mwa kuchita zosalungama.+

  • Malaki 3:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 “Anthu inu ndidzakuyandikirani kuti ndikuweruzeni.+ Sindidzazengereza kupereka umboni+ wotsutsa amatsenga,+ achigololo,+ olumbira monama+ komanso ochita chinyengo pa malipiro a munthu waganyu.+ Sindidzazengereza kupereka umboni wotsutsa anthu ochitira chinyengo mkazi wamasiye,+ mwana wamasiye*+ ndiponso opondereza alendo.+ Anthu amenewa sakundiopa,”+ watero Yehova wa makamu.

  • Yakobo 5:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Tamverani! Malipiro a anthu amene anagwira ntchito+ yokolola m’minda yanu, amene inu simunapereke,+ akufuula ndipo kufuula kwa okololawo kofuna thandizo+ kwafika m’makutu+ a Yehova wa makamu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena