Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 15:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Koma m’badwo wachinayi udzabwerera kuno,+ chifukwa nthawi yoti Aamori alangidwe sinakwane.”+

  • Genesis 28:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Ine ndili nawe ndipo ndikuyang’anira pa ulendo wako wonse, kufikira ndidzakubwezera kumalo ano.+ Sindidzakusiya kufikira nditachitadi zimene ndanena kwa iwe.”+

  • Genesis 47:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Tsopano nthawi inayandikira yakuti Isiraeli amwalire.+ Ndiye anaitana mwana wake Yosefe n’kumuuza kuti: “Ngati ungandikomere mtima, ika dzanja lako pansi pa ntchafu yanga.+ Ulumbire kuti udzandisonyeza kukoma mtima kosatha ndipo udzakhala wokhulupirika kwa ine.+ Chonde, usadzandiike m’manda ku Iguputo kuno.+

  • Genesis 50:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Anamunyamula n’kupita naye kudziko la Kanani. Kumeneko anakamuika m’phanga m’munda wa Makipela, woyang’anana ndi munda wa Mamure.+ Mundawo ndi umene Abulahamu anagula kwa Efuroni Mhiti, kuti akhale ndi manda.

  • Ekisodo 3:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Choncho nditsikira kwa iwo kuti ndiwalanditse m’manja mwa Aiguputo,+ ndi kuwatulutsa m’dzikolo, n’kuwalowetsa m’dziko labwino komanso lalikulu, dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ Ndiwalowetsa m’dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi.+

  • Salimo 105:37
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 37 Ndiyeno anayamba kuwatulutsa atatenga siliva ndi golide.+

      Pakati pa mafuko ake panalibe amene anapunthwa panjira.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena