-
Genesis 13:10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Choncho, Loti anakweza maso ake n’kuona Chigawo* chonse cha Yorodano+ mpaka kukafika ku Zowari,+ ndipo anaona kuti chinali chigawo chobiriwira bwino. Chinali chobiriwira bwino kwambiri ngati mmene unalili munda wa Yehova+ komanso ngati mmene linalili dziko la Iguputo. Pa nthawiyi n’kuti Yehova asanawononge Sodomu ndi Gomora.
-
-
Zefaniya 2:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Pali ine Mulungu wamoyo,+ Mowabu adzakhala ndendende ngati Sodomu,+ ndipo ana a Amoni+ adzakhala ngati Gomora, malo odzaza zomera zoyabwa ndiponso mchere ndiponso malo abwinja mpaka kalekale.*+ Otsala mwa anthu anga adzafunkha zinthu zawo, ndipo otsala a mtundu wa anthu anga adzawagwira ukapolo.+
-