Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 29:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Adzanena mawuwo akadzaonanso sulufule, mchere+ ndi kutentha,+ moti m’dzikomo simungabzalidwe mbewu, simungaphuke kalikonse ndipo simungamere chomera chilichonse, mofanana ndi Sodomu ndi Gomora,+ Adima+ ndi Zeboyimu,+ mizinda imene Yehova anaiwononga mu ukali ndi mkwiyo wake.+

  • Yesaya 13:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Babulo, amene ndi chokongoletsera maufumu,+ chinthu chokongola ndi chonyadira cha Akasidi,+ adzakhala ngati pamene Mulungu anagonjetsa Sodomu ndi Gomora.+

  • Yeremiya 50:40
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 40 “Monga mmene Mulungu anawonongera Sodomu ndi Gomora+ pamodzi ndi midzi yake yapafupi,+ dzikolo lidzawonongedwanso moti palibe munthu amene adzakhalanso mmenemo. Mwana wa munthu sadzakhalanso mmenemo ngati mlendo,”+ watero Yehova.

  • Yoweli 3:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Iguputo adzasanduka bwinja,+ Edomu adzasanduka chipululu chopanda kanthu+ chifukwa cha chiwawa chimene anachitira ana a Yuda, ndiponso chifukwa chokhetsa magazi osalakwa m’dziko la Yudalo.+

  • Yuda 7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Komanso mizinda ya Sodomu ndi Gomora ndi mizinda yozungulira mizinda imeneyi,+ inalandira chilango cha moto wosatha,+ motero yaikidwa monga chitsanzo chotichenjeza.+ Anthu ake anachita mofanana ndi amene tatchula aja, pochita dama loipitsitsa ndiponso pogonana m’njira imene si yachibadwa.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena