13 Koma Mose anafunsa Mulungu woona kuti: “Nditati ndakafika kwa ana a Isiraeli ndi kuwauza kuti, ‘Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu,’ iwo n’kundifunsa kuti, ‘Dzina lake ndani?’+ Ndikawayankhe kuti chiyani?”
3 Ndinali kuonekera kwa Abulahamu,+ Isaki+ ndi Yakobo+ monga Mulungu Wamphamvuyonse.+ Koma za dzina langa lakuti Yehova,+ ine sindinadzidziwikitse+ kwa iwo.