45 Poyankha Davide anauza Mfilisitiyo kuti: “Iwe ukubwera kwa ine ndi lupanga, mkondo ndi nthungo,+ koma ine ndikubwera kwa iwe m’dzina la Yehova wa makamu,+ Mulungu wa asilikali a Isiraeli, amene iweyo wam’tonza.+
9 Koma khamu la anthu, limene linali patsogolo pake ndi m’mbuyo mwake linali kufuula kuti: “M’pulumutseni+ Mwana wa Davide!+ Wodalitsidwa iye wobwera m’dzina la Yehova!*+ M’pulumutseni kumwambamwambako!”+