16 Koma Herode, poona kuti okhulupirira nyenyezi aja am’pusitsa, anakwiya koopsa. Choncho anatumiza anthu kukapha ana onse aamuna m’Betelehemu ndi m’zigawo zake zonse, kuyambira azaka ziwiri kutsika m’munsi, mogwirizana ndi nthawi imene anafunsira mosamala kwa okhulupirira nyenyezi aja.+