Ekisodo 4:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Yehova anauzanso Mose kuti: “Ukakafika ku Iguputo ukaonetsetse kuti wachita pamaso pa Farao,+ zozizwitsa zonse zimene ndakulola kukachita. Ndipo ine ndidzamusiya kuti aumitse mtima wake,+ moti sadzalola anthu anga kuchoka.+ Ekisodo 8:32 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 32 Koma pamenepanso, Farao anaumitsa mtima wake, ndipo sanalole anthuwo kuchoka.+ Ekisodo 14:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Koma ine ndilola Aiguputo kuumitsa mitima yawo,+ kuti atsatire Aisiraeli panyanjapo, kutinso ndipezerepo ulemerero mwa kugonjetsa Farao, magulu ake onse ankhondo, magaleta ake ankhondo ndi asilikali ake apamahatchi.+ Yoswa 11:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Yehova analola mitunduyo kuumitsa mitima+ yawo kuti ichite nkhondo ndi Aisiraeli. Anatero kuti iye awawononge ndi kuti Aisiraeliwo asawamvere chisoni,+ koma kuti awatheretu monga mmene Yehova analamulira Mose.+ 2 Mbiri 36:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Kuwonjezera pamenepo, Zedekiya anapandukira Mfumu Nebukadinezara+ yomwe inali itamulumbiritsa kwa Mulungu,+ ndipo anapitiriza kuumitsa khosi lake ndi mtima wake+ kuti asabwerere kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli. Salimo 75:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Musakweze nyanga yanu pamwamba.Musalankhule modzikuza.+
21 Yehova anauzanso Mose kuti: “Ukakafika ku Iguputo ukaonetsetse kuti wachita pamaso pa Farao,+ zozizwitsa zonse zimene ndakulola kukachita. Ndipo ine ndidzamusiya kuti aumitse mtima wake,+ moti sadzalola anthu anga kuchoka.+
17 Koma ine ndilola Aiguputo kuumitsa mitima yawo,+ kuti atsatire Aisiraeli panyanjapo, kutinso ndipezerepo ulemerero mwa kugonjetsa Farao, magulu ake onse ankhondo, magaleta ake ankhondo ndi asilikali ake apamahatchi.+
20 Yehova analola mitunduyo kuumitsa mitima+ yawo kuti ichite nkhondo ndi Aisiraeli. Anatero kuti iye awawononge ndi kuti Aisiraeliwo asawamvere chisoni,+ koma kuti awatheretu monga mmene Yehova analamulira Mose.+
13 Kuwonjezera pamenepo, Zedekiya anapandukira Mfumu Nebukadinezara+ yomwe inali itamulumbiritsa kwa Mulungu,+ ndipo anapitiriza kuumitsa khosi lake ndi mtima wake+ kuti asabwerere kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli.