Salimo 78:46 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 46 Anapereka zokolola zawo kwa mphemvu,Ndipo ntchito yawo yolemetsa anaipereka kwa dzombe.+ Salimo 105:34 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 34 Analamula kuti pagwe dzombe,+Ndipo panagwa dzombe losawerengeka la mtundu winawake.+ Miyambo 30:27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 Dzombe+ lilibe mfumu koma limauluka lonse litagawikana m’magulumagulu.+ Yoweli 1:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Zinthu zimene mbozi zinasiya zinadyedwa ndi dzombe.+ Zimene dzombelo linasiya zinadyedwa ndi ana a dzombe oyenda pansi opanda mapiko ndipo zimene ana a dzombe oyenda pansiwo anasiya zinadyedwa ndi mphemvu.+
4 Zinthu zimene mbozi zinasiya zinadyedwa ndi dzombe.+ Zimene dzombelo linasiya zinadyedwa ndi ana a dzombe oyenda pansi opanda mapiko ndipo zimene ana a dzombe oyenda pansiwo anasiya zinadyedwa ndi mphemvu.+