Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 12:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Ine ndidzatulutsa mtundu waukulu mwa iwe. Ndidzakudalitsa ndi kukuza dzina lako, ndipo iwe ukhale dalitso+ kwa ena.

  • Genesis 15:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Kenako anamutengera panja, n’kumuuza kuti: “Kweza maso ako kumwamba, uwerenge nyenyezizo ngati ungathe kuziwerenga.”+ Ndipo anamuuzanso kuti: “Umu ndi mmene mbewu yako idzakhalire.”+

  • Genesis 46:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Mulungu anapitiriza kuti: “Ine ndine Mulungu woona,+ Mulungu wa bambo ako.+ Usaope kupita ku Iguputo, chifukwa kumeneko ndidzakukuza kukhala mtundu waukulu.+

  • Ekisodo 1:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Ana a Isiraeli anaberekana ndipo anachuluka m’dzikomo. Iwo anapitiriza kuchulukana ndi kukhala amphamvu koposa, moti anadzaza m’dzikomo.+

  • Ekisodo 38:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Mwamuna aliyense amene anawerengedwa, kuyambira wa zaka 20 kupita m’tsogolo,+ anapereka hafu ya sekeli lolingana ndi hafu ya sekeli la kumalo oyera. Owerengedwa onse anakwana 603,550.+

  • Numeri 2:32
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 Amenewa ndiwo anali olembedwa mayina a ana a Isiraeli, malinga ndi nyumba ya makolo awo. Asilikali onse olembedwa mayina m’misasa yonse, analipo 603,550.+

  • Numeri 11:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Koma Mose anati: “Amuna amene ndikuyenda nawo akukwana 600,000,+ koma inuyo mukunena kuti, ‘Nyamayo ndiwapatsa, ndipo adzaidya kwa mwezi wonse wathunthu.’

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena