Genesis 15:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Kenako anamutengera panja, n’kumuuza kuti: “Kweza maso ako kumwamba, uwerenge nyenyezizo ngati ungathe kuziwerenga.”+ Ndipo anamuuzanso kuti: “Umu ndi mmene mbewu yako idzakhalire.”+ Ekisodo 12:37 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 37 Pamenepo ana a Isiraeli ananyamuka ku Ramese+ kupita ku Sukoti.+ Amuna amphamvu oyenda pansi analipo pafupifupi 600,000, osawerengera ana.+ Ekisodo 38:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Mwamuna aliyense amene anawerengedwa, kuyambira wa zaka 20 kupita m’tsogolo,+ anapereka hafu ya sekeli lolingana ndi hafu ya sekeli la kumalo oyera. Owerengedwa onse anakwana 603,550.+ Numeri 1:46 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 46 onse amene analembedwa mayina anakwana 603,550.+ Numeri 11:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Koma Mose anati: “Amuna amene ndikuyenda nawo akukwana 600,000,+ koma inuyo mukunena kuti, ‘Nyamayo ndiwapatsa, ndipo adzaidya kwa mwezi wonse wathunthu.’ Numeri 14:29 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 29 Mitembo yanu idzagona m’chipululu muno,+ nonsenu amene munawerengedwa, kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, inu amene mwakhala mukudandaula motsutsana nane.+ Numeri 26:51 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 51 Amenewa ndiwo amuna onse amene anawerengedwa pakati pa ana a Isiraeli. Onse pamodzi analipo 601,730.+
5 Kenako anamutengera panja, n’kumuuza kuti: “Kweza maso ako kumwamba, uwerenge nyenyezizo ngati ungathe kuziwerenga.”+ Ndipo anamuuzanso kuti: “Umu ndi mmene mbewu yako idzakhalire.”+
37 Pamenepo ana a Isiraeli ananyamuka ku Ramese+ kupita ku Sukoti.+ Amuna amphamvu oyenda pansi analipo pafupifupi 600,000, osawerengera ana.+
26 Mwamuna aliyense amene anawerengedwa, kuyambira wa zaka 20 kupita m’tsogolo,+ anapereka hafu ya sekeli lolingana ndi hafu ya sekeli la kumalo oyera. Owerengedwa onse anakwana 603,550.+
21 Koma Mose anati: “Amuna amene ndikuyenda nawo akukwana 600,000,+ koma inuyo mukunena kuti, ‘Nyamayo ndiwapatsa, ndipo adzaidya kwa mwezi wonse wathunthu.’
29 Mitembo yanu idzagona m’chipululu muno,+ nonsenu amene munawerengedwa, kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo, inu amene mwakhala mukudandaula motsutsana nane.+
51 Amenewa ndiwo amuna onse amene anawerengedwa pakati pa ana a Isiraeli. Onse pamodzi analipo 601,730.+