Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 13:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Ndidzachulukitsa mbewu yako ngati mchenga wa padziko lapansi, kotero kuti ngati munthu angathe kuwerenga mchengawo, ndiye kuti mbewu yako idzatha kuwerengedwa.+

  • Genesis 22:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 ndidzakudalitsa ndithu. Ndiponso ndidzachulukitsadi mbewu yako ngati nyenyezi zakumwamba, monganso mchenga wa m’mphepete mwa nyanja.+ Komanso mbewu yako idzalanda chipata* cha adani ake.+

  • Genesis 46:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Mulungu anapitiriza kuti: “Ine ndine Mulungu woona,+ Mulungu wa bambo ako.+ Usaope kupita ku Iguputo, chifukwa kumeneko ndidzakukuza kukhala mtundu waukulu.+

  • Ekisodo 12:37
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 37 Pamenepo ana a Isiraeli ananyamuka ku Ramese+ kupita ku Sukoti.+ Amuna amphamvu oyenda pansi analipo pafupifupi 600,000, osawerengera ana.+

  • Ekisodo 38:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Mwamuna aliyense amene anawerengedwa, kuyambira wa zaka 20 kupita m’tsogolo,+ anapereka hafu ya sekeli lolingana ndi hafu ya sekeli la kumalo oyera. Owerengedwa onse anakwana 603,550.+

  • Numeri 2:32
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 Amenewa ndiwo anali olembedwa mayina a ana a Isiraeli, malinga ndi nyumba ya makolo awo. Asilikali onse olembedwa mayina m’misasa yonse, analipo 603,550.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena