Ekisodo 14:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Ndiyeno mngelo+ wa Mulungu woona amene anali kuyenda patsogolo pa Aisiraeli anachoka n’kupita kumbuyo kwawo. Motero, mtambo woima njo ngati chipilala uja unachoka kutsogolo n’kukaima kumbuyo kwawo.+ Numeri 9:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Pa tsiku lomanga chihema chopatulika,+ mtambo unaima pamwamba pa chihema cha Umbonicho.+ Koma kuyambira madzulo mpaka m’mawa, moto+ unali kuoneka pamwamba pa chihema chopatulikacho. Deuteronomo 1:33 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 33 amene anali kutsogola kuti akuzondereni malo oti mumangepo msasa wanu.+ Usiku anali kukutsogolerani ndi moto kuti muziona njira yoyendamo, ndipo masana anali kukutsogolerani ndi mtambo.+ Nehemiya 9:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Usana munali kuwatsogolera ndi mtambo woima njo ngati chipilala,+ ndipo usiku munali kuwatsogolera ndi moto woima njo ngati chipilala+ kuti uziwaunikira+ njira imene anayenera kuyendamo. Salimo 99:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Mulungu anapitiriza kulankhula nawo mumtambo woima njo ngati chipilala.+Iwo anasunga zikumbutso zake ndi malangizo amene anawapatsa.+
19 Ndiyeno mngelo+ wa Mulungu woona amene anali kuyenda patsogolo pa Aisiraeli anachoka n’kupita kumbuyo kwawo. Motero, mtambo woima njo ngati chipilala uja unachoka kutsogolo n’kukaima kumbuyo kwawo.+
15 Pa tsiku lomanga chihema chopatulika,+ mtambo unaima pamwamba pa chihema cha Umbonicho.+ Koma kuyambira madzulo mpaka m’mawa, moto+ unali kuoneka pamwamba pa chihema chopatulikacho.
33 amene anali kutsogola kuti akuzondereni malo oti mumangepo msasa wanu.+ Usiku anali kukutsogolerani ndi moto kuti muziona njira yoyendamo, ndipo masana anali kukutsogolerani ndi mtambo.+
12 Usana munali kuwatsogolera ndi mtambo woima njo ngati chipilala,+ ndipo usiku munali kuwatsogolera ndi moto woima njo ngati chipilala+ kuti uziwaunikira+ njira imene anayenera kuyendamo.
7 Mulungu anapitiriza kulankhula nawo mumtambo woima njo ngati chipilala.+Iwo anasunga zikumbutso zake ndi malangizo amene anawapatsa.+