Ekisodo 7:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Koma ine ndidzamusiya Farao kuti aumitse mtima wake,+ ndipo ndidzachita zizindikiro ndi zozizwitsa zochuluka m’dziko la Iguputo.+ Deuteronomo 2:30 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 30 Koma Sihoni mfumu ya Hesiboni sanatilole kudutsa m’dziko lake, chifukwa Yehova Mulungu wanu anamulola kuti akhale wokanika+ ndi kuti aumitse mtima wake. Anatero kuti am’pereke m’manja mwanu monga mmene zilili lero.+ Yoswa 11:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Yehova analola mitunduyo kuumitsa mitima+ yawo kuti ichite nkhondo ndi Aisiraeli. Anatero kuti iye awawononge ndi kuti Aisiraeliwo asawamvere chisoni,+ koma kuti awatheretu monga mmene Yehova analamulira Mose.+ Salimo 10:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Modzikweza, woipa amathamangitsa wosautsika,+Ndipo wosautsikayo amakodwa ndi maganizo amene woipa walingalira.+ Miyambo 16:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Kunyada kumafikitsa munthu ku chiwonongeko,+ ndipo mtima wodzikuza umachititsa munthu kupunthwa.+
3 Koma ine ndidzamusiya Farao kuti aumitse mtima wake,+ ndipo ndidzachita zizindikiro ndi zozizwitsa zochuluka m’dziko la Iguputo.+
30 Koma Sihoni mfumu ya Hesiboni sanatilole kudutsa m’dziko lake, chifukwa Yehova Mulungu wanu anamulola kuti akhale wokanika+ ndi kuti aumitse mtima wake. Anatero kuti am’pereke m’manja mwanu monga mmene zilili lero.+
20 Yehova analola mitunduyo kuumitsa mitima+ yawo kuti ichite nkhondo ndi Aisiraeli. Anatero kuti iye awawononge ndi kuti Aisiraeliwo asawamvere chisoni,+ koma kuti awatheretu monga mmene Yehova analamulira Mose.+
2 Modzikweza, woipa amathamangitsa wosautsika,+Ndipo wosautsikayo amakodwa ndi maganizo amene woipa walingalira.+