Numeri 14:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Koma anthu onse amene aona ulemerero wanga,+ ndi zizindikiro zanga+ zimene ndinachita ku Iguputo, ndi zimene ndachita m’chipululu, amene akupitirizabe kundiyesa+ maulendo 10 onsewa, amenenso sanamvere mawu anga,+ Salimo 78:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Iwo anapitiriza kuyesa Mulungu m’mitima yawo+Mwa kupempha chakudya china chimene mtima wawo unalakalaka.+ Salimo 95:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Pamene makolo anu anandiyesa.+Iwo anandisanthula, ndipo anaonanso ntchito zanga.+ Salimo 106:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Anasonyeza chikhumbo chawo chadyera m’chipululu,+Ndipo anayesa Mulungu m’chipululumo.+ Luka 4:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Poyankha Yesu anamuuza kuti: “Pajatu Malemba amati, ‘Usamuyese, Yehova Mulungu wako.’”+ 1 Akorinto 10:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Kapena tisamuyese Yehova,+ mmene ena mwa iwo anamuyesera,+ n’kuwonongeka polumidwa ndi njoka.+ Aheberi 3:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 M’chipululumo, makolo anu anandiyesa ndi mayesero, ngakhale kuti anali ataona ntchito zanga+ kwa zaka 40.+
22 Koma anthu onse amene aona ulemerero wanga,+ ndi zizindikiro zanga+ zimene ndinachita ku Iguputo, ndi zimene ndachita m’chipululu, amene akupitirizabe kundiyesa+ maulendo 10 onsewa, amenenso sanamvere mawu anga,+
18 Iwo anapitiriza kuyesa Mulungu m’mitima yawo+Mwa kupempha chakudya china chimene mtima wawo unalakalaka.+
9 M’chipululumo, makolo anu anandiyesa ndi mayesero, ngakhale kuti anali ataona ntchito zanga+ kwa zaka 40.+