14 “Tsopano opani Yehova+ ndi kum’tumikira mosalakwitsa ndiponso mokhulupirika.*+ Chotsani milungu imene makolo anu ankatumikira kutsidya lina la Mtsinje ndi ku Iguputo,+ ndipo tumikirani Yehova.
13 Yehova wa makamu ndi amene muyenera kumuona kuti ndi woyera,+ ndipo iyeyo ndi amene muyenera kumuopa.+ Iye ndi amene ayenera kukuchititsani kunjenjemera.”+