Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 18:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Amenewa ndiwo aziweruza anthu pa nkhani iliyonse yoyenera. Ndiyeno pakakhala nkhani iliyonse yaikulu azibwera nayo kwa iwe,+ koma nkhani iliyonse yaing’ono, iwo monga oweruza aziisamalira. Choncho amunawo athandizane nawe kunyamula mtolowu, kuti udzipeputsire ntchito.+

  • Deuteronomo 16:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 “Mudziikire oweruza+ ndi atsogoleri+ m’mizinda yanu yonse imene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, malinga ndi mafuko anu. Oweruza ndi atsogoleriwo aziweruza anthu ndi chiweruzo cholungama.

  • Deuteronomo 25:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 “Amuna akakangana+ n’kupita kwa oweruza,+ oweruzawo azigamula mlanduwo. Wolungama azimuweruza kuti ndi wolungama ndipo woipa azimuweruza kuti ndi woipa.+

  • 1 Samueli 2:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Munthu akachimwira mnzake,+ Mulungu adzam’pepesera,+ koma kodi akachimwira Yehova,+ angamupempherere ndani?”+ Koma anawo sanali kumvera bambo awo+ chifukwa tsopano Yehova anali atatsimikiza mtima kuti awaphe.+

  • 2 Mbiri 19:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Pa mlandu uliwonse wobwera kwa inu kuchokera kwa abale anu amene akukhala m’mizinda yawo, wokhudza kukhetsa magazi,+ chilamulo,+ ndi zigamulo,+ muziwachenjeza kuti asalakwire Yehova kuopera kuti mkwiyo wa Mulungu+ ungakuyakireni inuyo ndi abale anu. Muzichita zimenezi n’cholinga choti musapalamule mlandu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena