6 Nsembe zanu zopsereza+ ndi nsembe zina, zopereka zanu za chakhumi,*+ chopereka chochokera m’manja mwanu,+ nsembe zanu za lonjezo,+ nsembe zanu zaufulu,+ ana oyamba kubadwa a ng’ombe ndi a nkhosa zanu,+ zonsezi muzidzazibweretsa kumalo amenewo.
8 Akalonga ake+ anapereka nsembe yaufulu kwa anthuwo,+ kwa ansembe ndi kwa Alevi. Hilikiya,+ Zekariya ndi Yehiela monga atsogoleri a nyumba ya Mulungu woona, anapereka kwa ansembe nkhosa ndi mbuzi zokwana 2,600 ndiponso ng’ombe 300 kuti zikhale nyama zophera pasika.
68 Atsogoleri ena+ a nyumba za makolo awo+ atafika kunyumba ya Yehova+ imene inali ku Yerusalemu,+ anapereka zopereka zaufulu+ kunyumba ya Mulungu woona kuti imangidwe pamalo ake.+