Oweruza 5:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 M’masiku a Samagara+ mwana wa Anati,M’masiku a Yaeli,+ m’njira munalibe odutsamo,Ndipo oyenda m’misewu anayamba kuyenda njira zolambalala.+ Yesaya 33:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Misewu ikuluikulu yawonongeka.+ Palibenso munthu woyenda m’njira.+ Iye waphwanya pangano+ ndipo wanyansidwa ndi mizinda.+ Sasamala za munthu aliyense.+ Ezekieli 14:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 “‘Nditati ndichititse zilombo zolusa zakutchire kudutsa m’dzikolo,+ zilombozo n’kuliphera ana dzikolo,+ moti dzikolo n’kukhala bwinja lokhalokha popanda munthu aliyense wodutsamo chifukwa cha zilombo zolusazo,+ Zekariya 7:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 ‘Chotero ndinawabalalitsira ku mitundu yonse ya anthu+ imene sanali kuidziwa,+ ngati kuti atengedwa ndi mphepo yamkuntho. Dzikoli analisiya labwinja, popanda munthu wodutsamo kapena kuyendayendamo.+ Iwo anasandutsa dziko losiririka+ kukhala chinthu chodabwitsa.’”
6 M’masiku a Samagara+ mwana wa Anati,M’masiku a Yaeli,+ m’njira munalibe odutsamo,Ndipo oyenda m’misewu anayamba kuyenda njira zolambalala.+
8 Misewu ikuluikulu yawonongeka.+ Palibenso munthu woyenda m’njira.+ Iye waphwanya pangano+ ndipo wanyansidwa ndi mizinda.+ Sasamala za munthu aliyense.+
15 “‘Nditati ndichititse zilombo zolusa zakutchire kudutsa m’dzikolo,+ zilombozo n’kuliphera ana dzikolo,+ moti dzikolo n’kukhala bwinja lokhalokha popanda munthu aliyense wodutsamo chifukwa cha zilombo zolusazo,+
14 ‘Chotero ndinawabalalitsira ku mitundu yonse ya anthu+ imene sanali kuidziwa,+ ngati kuti atengedwa ndi mphepo yamkuntho. Dzikoli analisiya labwinja, popanda munthu wodutsamo kapena kuyendayendamo.+ Iwo anasandutsa dziko losiririka+ kukhala chinthu chodabwitsa.’”