Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 17:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Munthu aliyense amene wadya nyama imene waipeza yakufa, kapena yophedwa ndi chilombo,+ kaya akhale nzika kapena mlendo wokhala pakati panu, munthu ameneyo azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo.+ Kenako azikhala woyera.

  • Levitiko 22:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Iye asadye nyama iliyonse imene waipeza yakufa, kapena iliyonse yophedwa ndi zilombo, chifukwa angakhale wodetsedwa.+ Ine ndine Yehova.

  • Deuteronomo 14:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 “Musadye nyama iliyonse imene mwaipeza yakufa.+ Muziipereka kwa mlendo wokhala mumzinda wanu kuti adye, kapena muziigulitsa kwa mlendo* chifukwa inu ndinu anthu oyera kwa Yehova Mulungu wanu.

      “Musawiritse mwana wa mbuzi mumkaka wa mayi wake.+

  • Ezekieli 4:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Kenako ine ndinati: “Chonde Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ine sindine woipitsidwa.+ Sindinadyepo nyama yopezeka itafa kapena nyama yochita kukhadzulidwa ndi chilombo kuyambira ndili mwana+ mpaka panopo, ndipo m’kamwa mwanga simunalowepo nyama yodetsedwa.”+

  • Ezekieli 44:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Ansembe asamadye nyama iliyonse imene aipeza yakufa, asamadye chouluka chilichonse kapena nyama iliyonse imene yakhadzulidwa ndi chilombo.’+

  • Machitidwe 10:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Pamenepo mawu anamveka kwa iye kuti: “Nyamuka Petulo, ipha udye!”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena