Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 53:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Tonsefe tinkangoyendayenda uku ndi uku ngati nkhosa.+ Aliyense analowera njira yake ndipo Yehova wachititsa cholakwa cha aliyense wa ife kugwera pa ameneyo.+

  • Maliko 10:45
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 45 Pakuti ngakhale Mwana wa munthu sanabwere kudzatumikiridwa,+ koma kudzatumikira ndi kudzapereka moyo wake dipo+ kuwombola anthu ambiri.”+

  • Aheberi 2:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Koma tikuona Yesu, amene pa nthawi ina anamutsitsa pang’ono poyerekeza ndi angelo.+ Tikumuona atamuveka ulemerero+ ndi ulemu ngati chisoti chachifumu chifukwa chakuti anazunzika mpaka imfa.+ Zimenezi zinamuchitikira kuti mwa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, alawe imfa m’malo mwa munthu aliyense.+

  • Aheberi 9:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Koma m’chipinda chachiwiricho, mkulu wa ansembe yekha ndiye anali kulowamo kamodzi pa chaka,+ ndipo sanali kulowamo popanda kutenga magazi.+ Magaziwo anali kuwapereka chifukwa cha iye mwini,+ komanso chifukwa cha machimo a anthu amene anachita mosadziwa.+

  • Aheberi 9:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Choncho iye analowa m’malo oyera amkatikati ndi magazi+ ake, osati ndi magazi a mbuzi kapena a ng’ombe zazing’ono zamphongo. Analowa kamodzi kokha m’malo oyera amkatikatiwo, ndipo anatilanditsa kwamuyaya.+

  • 1 Yohane 2:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Iye ndi nsembe+ yophimba+ machimo athu.+ Osati athu+ okha, komanso a dziko lonse lapansi.+

  • Chivumbulutso 1:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Komanso, kuchokera kwa Yesu Khristu, “Mboni Yokhulupirika,”+ “Woyamba kubadwa kuchokera kwa akufa,”+ ndiponso “Wolamulira wa mafumu a dziko lapansi.”+

      Kwa iye amene amatikonda,+ amenenso anatimasula ku machimo athu ndi magazi ake enieniwo,+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena