Ekisodo 15:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Mudzawabweretsa ndi kuwakhazikitsa m’phiri limene ndi cholowa chanu.+Malo okhazikika amene mwakonzeratu kuti mukakhalemo,+ inu Yehova.Malo opatulika+ amene manja anu, inu Yehova, anakhazikitsa. Numeri 19:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 “‘Koma munthu wodetsedwa akapanda kudziyeretsa, ameneyo aphedwe+ kuti asakhalenso pakati pa mpingowo, chifukwa waipitsa malo opatulika a Yehova. Iye sanawazidwe madzi oyeretsera. Choncho ndi wodetsedwa. Deuteronomo 23:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Pakuti Yehova Mulungu wanu akuyendayenda mumsasa wanu kuti akulanditseni+ ndi kupereka adani anu m’manja mwanu.+ Choncho msasa wanu uzikhala woyera,+ kuti asaone choipa chilichonse pakati panu ndi kutembenuka n’kuleka kuyenda nanu limodzi.+ Ezekieli 5:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pali ine Mulungu wamoyo, chifukwa chakuti iwe unaipitsa malo anga opatulika ndi mafano ako onse onyansa+ ndi zinthu zako zonse zonyansa,+ ndithu ineyo ndidzakuchepetsa.+ Diso langa silidzakumvera chisoni+ ndipo sindidzakuchitira chifundo.+
17 Mudzawabweretsa ndi kuwakhazikitsa m’phiri limene ndi cholowa chanu.+Malo okhazikika amene mwakonzeratu kuti mukakhalemo,+ inu Yehova.Malo opatulika+ amene manja anu, inu Yehova, anakhazikitsa.
20 “‘Koma munthu wodetsedwa akapanda kudziyeretsa, ameneyo aphedwe+ kuti asakhalenso pakati pa mpingowo, chifukwa waipitsa malo opatulika a Yehova. Iye sanawazidwe madzi oyeretsera. Choncho ndi wodetsedwa.
14 Pakuti Yehova Mulungu wanu akuyendayenda mumsasa wanu kuti akulanditseni+ ndi kupereka adani anu m’manja mwanu.+ Choncho msasa wanu uzikhala woyera,+ kuti asaone choipa chilichonse pakati panu ndi kutembenuka n’kuleka kuyenda nanu limodzi.+
11 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pali ine Mulungu wamoyo, chifukwa chakuti iwe unaipitsa malo anga opatulika ndi mafano ako onse onyansa+ ndi zinthu zako zonse zonyansa,+ ndithu ineyo ndidzakuchepetsa.+ Diso langa silidzakumvera chisoni+ ndipo sindidzakuchitira chifundo.+