Ekisodo 19:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Tsopano ngati mudzalabadiradi+ mawu anga ndi kusunga pangano langa,+ pamenepo mudzakhaladi chuma changa chapadera pakati pa anthu ena onse,+ chifukwa dziko lonse lapansi ndi langa.+ Ekisodo 33:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Ndipo ndidziwa bwanji kuti mwandikomera mtima, ineyo ndi anthu anu? Si mwa kuyenda nafe kodi?+ Pajatu ine ndi anthu anu mwatisiyanitsa ndi anthu ena onse amene ali padziko lapansi.”+ 1 Mafumu 8:53 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 53 Pakuti inuyo munawapatula pakati pa mitundu yonse ya anthu a padziko lapansi+ kuti akhale cholowa chanu, monga momwe munalankhulira kudzera mwa Mose+ mtumiki wanu, pamene munali kutulutsa makolo athu ku Iguputo, inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa.” 2 Akorinto 6:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Ndipo pali kumvana kotani pakati pa kachisi wa Mulungu ndi mafano?+ Pakuti ifeyo ndife kachisi+ wa Mulungu wamoyo, monga ananenera Mulungu kuti: “Ndidzakhala pakati pawo+ ndi kuyenda pakati pawo. Ndidzakhala Mulungu wawo, ndipo iwo adzakhala anthu anga.”+ 1 Petulo 2:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Koma inu ndinu “fuko losankhidwa mwapadera, ansembe achifumu, mtundu woyera,+ anthu odzakhala chuma chapadera,+ kuti mulengeze makhalidwe abwino kwambiri”+ a amene anakuitanani kuchoka mu mdima kulowa m’kuwala kwake kodabwitsa.+
5 Tsopano ngati mudzalabadiradi+ mawu anga ndi kusunga pangano langa,+ pamenepo mudzakhaladi chuma changa chapadera pakati pa anthu ena onse,+ chifukwa dziko lonse lapansi ndi langa.+
16 Ndipo ndidziwa bwanji kuti mwandikomera mtima, ineyo ndi anthu anu? Si mwa kuyenda nafe kodi?+ Pajatu ine ndi anthu anu mwatisiyanitsa ndi anthu ena onse amene ali padziko lapansi.”+
53 Pakuti inuyo munawapatula pakati pa mitundu yonse ya anthu a padziko lapansi+ kuti akhale cholowa chanu, monga momwe munalankhulira kudzera mwa Mose+ mtumiki wanu, pamene munali kutulutsa makolo athu ku Iguputo, inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa.”
16 Ndipo pali kumvana kotani pakati pa kachisi wa Mulungu ndi mafano?+ Pakuti ifeyo ndife kachisi+ wa Mulungu wamoyo, monga ananenera Mulungu kuti: “Ndidzakhala pakati pawo+ ndi kuyenda pakati pawo. Ndidzakhala Mulungu wawo, ndipo iwo adzakhala anthu anga.”+
9 Koma inu ndinu “fuko losankhidwa mwapadera, ansembe achifumu, mtundu woyera,+ anthu odzakhala chuma chapadera,+ kuti mulengeze makhalidwe abwino kwambiri”+ a amene anakuitanani kuchoka mu mdima kulowa m’kuwala kwake kodabwitsa.+