11 Ndipo ena mwa inu munali otero.+ Koma mwasambitsidwa kukhala oyera,+ mwapatulidwa,+ mwayesedwa olungama+ m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu,+ komanso ndi mzimu wa Mulungu wathu.+
13 Pakuti ngati magazi a mbuzi+ ndi a ng’ombe zamphongo+ komanso phulusa+ la ng’ombe yaikazi imene sinaberekepo, zimene amawaza nazo anthu oipitsidwa,+ zimawayeretsa mpaka kukhaladi oyera pamaso pa Mulungu,+