Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 31:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 “Koma iwe uuze ana a Isiraeli kuti, ‘Muonetsetse kuti muzisunga masiku anga a sabata,+ pakuti ndi chizindikiro pakati pa ine ndi inu m’mibadwo yanu yonse, kuti mudziwe kuti ine Yehova ndakusankhani kukhala opatulika.+

  • Levitiko 21:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Choncho muzim’patula+ chifukwa ndiye wopereka mkate wa Mulungu wanu. Azikhala woyera kwa inu,+ chifukwa ine Yehova, amene ndikukupatulani, ndine woyera.+

  • Ezekieli 37:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Malo anga opatulika akadzakhala pakati pawo mpaka kalekale, mitundu ina ya anthu idzadziwa kuti ine Yehova+ ndikuyeretsa Isiraeli.”’”+

  • 1 Atesalonika 5:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Mulungu wamtendere+ mwiniyo akupatuleni+ kuti muchite utumiki wake. Ndipo m’mbali zonse abale, mzimu wanu, moyo wanu, ndi thupi lanu, zisungidwe zopanda chilema ndi zopanda cholakwa chilichonse, pa nthawi ya kukhalapo* kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.+

  • 2 Atesalonika 2:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Komabe, tiyeneradi kumayamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu abale okondedwa ndi Yehova. Tiyenera kutero chifukwa Mulungu anakusankhani+ kuchokera pachiyambi kuti mudzapulumuke mwa kukuyeretsani+ ndi mzimu,+ ndiponso mwa chikhulupiriro chanu m’choonadi.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena