52 “Ana a Isiraeli azimanga mahema awo, aliyense malinga ndi msasa wawo, munthu aliyense malinga ndi gulu lake la mafuko atatu,+ malinga ndi magulu awo a asilikali.
2 “Ana a Isiraeli azikhoma mahema awo, aliyense azikhoma hema wake m’chigawo chawo cha mafuko atatu,+ potsata chizindikiro cha nyumba ya makolo ake. Azikhoma mahema awo mozungulira chihema chokumanako komanso moyang’ana chihemacho.