20 Nthawi yomweyo, Sauli anatumiza amithenga kuti akagwire Davide. Amithengawo ataona aneneri achikulire akunenera, Samueli ataima pakati pawo kuwatsogolera, mzimu+ wa Mulungu unafika pa amithenga a Sauli aja, ndipo nawonso anayamba kuchita zinthu ngati aneneri.+