38 zofukizira za amuna amene anafa+ chifukwa cha kuchimwa. Azisule kuti zikhale timalata topyapyala n’kukutira nato guwa lansembe,+ popeza anafika nazo pamaso pa Yehova, ndipo zakhala zopatulika. Timalatato tikhale chikumbutso kwa ana a Isiraeli.’”+
6 Anaweruzanso mizinda ya Sodomu ndi Gomora mwa kuinyeketsa ndi moto,+ kuti chikhale chitsanzo cha zinthu zimene zidzachitikire anthu osaopa Mulungu m’tsogolo.+