16 Komanso muzichita chikondwerero cha zokolola, chokondwerera zipatso za ntchito ya manja anu zoyamba kucha+ zimene munabzala m’munda.+ Muzichitanso chikondwerero cha kututa kumapeto kwa chaka, pamene mututa zipatso za manja anu, zam’munda.+
14 Pamenepo anapeza kuti m’chilamulo chimene Yehova anawapatsa kudzera mwa Mose+ analembamo kuti ana a Isiraeli azikhala m’misasa+ pa nthawi ya chikondwerero m’mwezi wa 7.+