Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 23:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Komanso muzichita chikondwerero cha zokolola, chokondwerera zipatso za ntchito ya manja anu zoyamba kucha+ zimene munabzala m’munda.+ Muzichitanso chikondwerero cha kututa kumapeto kwa chaka, pamene mututa zipatso za manja anu, zam’munda.+

  • Numeri 29:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 “‘Pa tsiku la 15 la mwezi wa 7,+ muzichita msonkhano wopatulika.+ Musamagwire ntchito yolemetsa yamtundu uliwonse.+ Muzichita chikondwerero kwa Yehova masiku 7.+

  • Deuteronomo 16:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 “Uzichita chikondwerero cha misasa+ masiku 7, potuta zokolola kuchokera pamalo opunthira mbewu, pamalo oyengera mafuta ndi pamalo opondera mphesa.

  • Ezara 3:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Kenako iwo anachita chikondwerero cha misasa+ mogwirizana ndi zimene zinalembedwa.+ Pachikondwererochi, anthuwo anali kubweretsa nsembe zopsereza paguwa lansembe tsiku ndi tsiku, mogwirizana ndi lamulo la nsembe zimene zinayenera kuperekedwa tsiku lililonse.+

  • Nehemiya 8:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Pamenepo anapeza kuti m’chilamulo chimene Yehova anawapatsa kudzera mwa Mose+ analembamo kuti ana a Isiraeli azikhala m’misasa+ pa nthawi ya chikondwerero m’mwezi wa 7.+

  • Zekariya 14:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 “Aliyense wotsala mwa anthu a mitundu yonse amene akubwera kudzamenyana ndi Yerusalemu,+ azidzapita kukagwadira Mfumu,+ Yehova wa makamu,+ chaka ndi chaka,+ ndi kukachita nawo chikondwerero cha misasa.+

  • Yohane 7:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Komabe chikondwerero cha Ayuda, chikondwerero cha misasa+ chinali pafupi.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena