19 Pakuti ana a anthu ali ndi mapeto, ndipo zinyamanso zili ndi mapeto. Mapeto a zonsezi ndi ofanana.+ Nyama imafa ndipo munthunso amafa.+ Mzimu wa zonsezi ndi umodzi,+ moti munthu saposa nyama, pakuti zonse n’zachabechabe.
“Awa ndi mawu a Yehova okhudza Isiraeli.” Yehova, amene anatambasula miyamba+ ndi kuyala maziko a dziko lapansi+ komanso kupanga mzimu+ n’kuuika mwa munthu, wanena kuti: