8 Tsoka ife! Adzatipulumutsa ndani m’manja mwa Mulungu wamkuluyu? Ameneyu ndi Mulungu amene anakantha Iguputo ndi masautso amtundu uliwonse m’chipululu.+
3 Aliyense amene ali pakati panu mwa anthu onse amene amamutumikira, Mulungu wake akhale naye.+ Choncho apite ku Yerusalemu m’dziko la Yuda n’kukamanganso nyumba ya Yehova Mulungu wa Isiraeli, yomwe inali ku Yerusalemu.+ Iye ndiye Mulungu woona.+