Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 32:35
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 Kubwezera ndi kwanga, chilangonso ndi changa.+

      Pa nthawi yoikidwiratu phazi lawo lidzaterereka poyenda,+

      Pakuti tsiku la tsoka lawo layandikira,+

      Ndipo zowagwera zikufika mofulumira.’+

  • Yesaya 1:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Choncho mawu a Ambuye woona, Yehova wa makamu, Wamphamvu wa Isiraeli,+ ndi akuti: “Eya! Ndidzibweretsera mpumulo pochotsa adani anga ndipo ndibwezera+ odana nane.+

  • Yesaya 59:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Iye adzawapatsa mphoto mogwirizana ndi zochita zawo.+ Adani ake adzawapatsa mkwiyo ndipo anthu otsutsana naye adzawapatsa chilango chowayenerera.+ Zilumbanso adzazipatsa chilango choyenerera.+

  • Yesaya 66:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Mumzinda mukumveka phokoso lachisokonezo, phokoso lochokera kukachisi.+ Limeneli ndi phokoso losonyeza kuti Yehova akubwezera adani ake chilango chowayenerera.+

  • Nahumu 1:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Yehova ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha+ ndipo amabwezera adani ake.+ Yehova amabwezera adani ake ndipo ndi waukali.+ Yehova amabwezera adani ake+ ndipo saiwala zoipa zimene iwo anachita.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena